Home Sports WAYAMBA NAWO ZOKOZEKERA -MPACHIKA

WAYAMBA NAWO ZOKOZEKERA -MPACHIKA

by Archangel Palasido
0 comments

Osewera wakale wa timu ya Dedza Young Soccer Chisomo Mpachika wa m’boma la Dedza ndi m’modzi mwa osewera omwe awoneka kuzokonzekera zoyamba za timu ya Masters Security FC.
Mpachika yemwe wakhala nthawi yayitali ali ndi timu ya Silver Strikers, ndi m’modzi mwa osewera odziwika bwino omwe mphunzitsi wakale wa matimu a Silver Strikers komanso FCB Nyasa Big Bullets Peter Mponda yemwe akutsogolera timu ya Masters padakali pano anawafuna kuti akhale nawo ku timuyi.
Timu ya Masters Security FC ikubweleranso mu ligi yayikulu m’dziko muno itagula malo osewera mu ligiyi kuchoka ku timu ya Baka City ya m’chigawo chakumpoto.

Leave a Comment

Radio Bembeke 100.0FM is a non-profit making media house licensed with the Registrar Of Companies

Newsletter

Subscribe my Newsletter for new blog posts, tips & new photos. Let's stay updated!

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00